Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 7:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.

6. Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magareta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikuru; nanenana wina ndi mnzace, Taonani mfumu ya Israyeli watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aaigupto, atigwere.

7. Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi aburu ao, misasa iri cimangire; nathawa, apulumutse moyo wao.

8. Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.

9. Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.

10. Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi aburu omanga, ndi mahema ali cimangire.

11. Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m'nyumba ya mfumu.

12. Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ace, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu aticitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, laturuka m'misasa, nabisala kuurengo, ndi kuti, Pamene aturuka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo.

13. Nayankha mmodzi wa anyamata ace, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israyeli otsirizika; tiwatumize tione.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 7