Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:2-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.

3. Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wace ndiye Abigayeli; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa macitidwe ace; ndipo iye anali wa banja la Kalebi.

4. Ndipo Davide anamva kucipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zace.

5. Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimeli, mumuke kwa Nabala ndi kundilankhulira iye;

6. ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.

7. Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawacititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimeli.

8. Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; cifukwa cace muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tirikufika tsiku labwino; mupatse ciri conse muli naco m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.

9. Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka.

10. Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? ndi mwana walese ndani? Makono ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.

11. Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

12. Comweco anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.

13. Ndipo Davide anati kwa anthu ace, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lace. Namangirira munthu yense lupanga lace; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lace; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

14. Koma mnyamata wina anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akucokera kucipululu kulankhula mbuye wathu; koma iye anawakalipira.

15. Koma anthu aja anaticitira zabwino ndithu, sanaticititsa manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja;

16. iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.

17. Cifukwa cace tsono mudziwe ndi kulingalira cimene mudzacita; popeza anatsimikiza mtima kucitira coipa mbuye wathu, ndi nyumba yace yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.

18. Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.

19. Nati kwa anyamataace, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuvo mwanu. Koma sanauza mwamuna wace Nabala.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25