Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:47-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m'manja athu.

48. Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

49. Ndipo Davide anapisa dzanja lace m'thumba mwace, naturutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi cafufumimba.

50. Comweco Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa coponyera cace, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.

51. Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lace, nalisolola m'cimace, namtsiriza nadula nalo mutu wace. Ndipo pakuona Afilisti kuti ciwinda cao cidafa, anathawa.

52. Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.

53. Ndipo ana a Israyeli atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.

54. Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zace anazisunga m'hema wace.

55. Ndipo pamene Sauli anaona Davide alikuturukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abineri, kazembe wa khamu la nkhondo, Abineri, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abineri, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.

56. Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani.

57. Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abineri anamtenga, nafika naye pamaso pa Sauli, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lace.

58. Ndipo Sauli anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndiri mwana wa kapolo wanu Jese wa ku Betelehemu.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17