Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 5:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebano, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.

7. Ndipo kunacitika, pamene Hiramu anamva mau ace a Solomo, anakondwera kwakukuru, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.

8. Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomo, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzacita cifuniro canu conse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa.

9. Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebano kufika nayo ku nyanja yamcere, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzacita cifuniro canga, kumapatsa banja langa zakudya.

10. Tsono Hiramu anapatsa Solomo mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo.

11. Ndipo Solomo anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lace, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomo anapatsa Hiramu caka ndi caka.

12. Ndipo Yehova anapatsa Solomo nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomo, iwo awiri napangana pamodzi.

13. Ndipo mfumu Solomo anasonkhetsa athangata mwa Aisrayeli onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu.

14. Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.

15. Ndipo Solomo anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri;

16. osawerenga akapitao a Solomo akuyang'anira nchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira nchito.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 5