Ndipo kunacitika, pamene Hiramu anamva mau ace a Solomo, anakondwera kwakukuru, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.