Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:24-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Tsono citani ici, cotsani mafumu aja yense ku malo ace, muike m'malo mwao akazembe.

25. Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magareta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pacidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.

26. Tsono kunacitika, pakufikanso caka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Meld kukaponyana ndi Aisrayeli.

27. Ndipo Aisrayeli anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisrayeli anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta ana a mbuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.

28. Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israyeli, nati, Atero: Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ici ndidzapereka unyinji uwu waukuru m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29. Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30. Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.

31. Pamenepo anyamata ace anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israyeli ndi mafumu acifundo; tiyeni tibvale ciguduli m'cuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titurukire kwa mfumu ya Israyeli, kapena adzakusungirani moyo.

32. Motero anabvala ciguduli m'cuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israyeli, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.

33. Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni, Pamenepo Benihadadi anaturuka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'gareta mwaceo

34. Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samaria. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.

35. Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzace mwa mau a Yehova, Undikanthe ine, Koma munthuyo anakana kumkantha.

36. Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha, Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.

37. Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.

38. Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pace.

39. Ndipo popitapa mfumu, anapfuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapambuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi cifukwa ciri conse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wace, kapena udzalipa talenti la siliva.

40. Tsono pocita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.

41. Ndipo iye anafulumira kucotsa mpango kumaso kwace, ndi mfumu ya Israyeli inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20