Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 19:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Ahabu anauza Yezebeli zonse anazicita Eliya, ndi m'mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo,

2. Tsono Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe yino.

3. Ndipo iye ataona cimeneci, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wace pamenepo.

4. Koma iye mwini analowa m'cipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, cotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.

5. Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.

6. Ndipo anaceuka, naona kumutu kunali kamkate kooca pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi,

7. Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kaciwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka.

8. Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvuya cakudya cimeneco masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika ku phiri la Mulungu ku Horebu.

9. Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Ucitanji pano, Eliya?

10. Ndipo anati, Ine ndinacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli anasiya cipangano canu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.

11. Ndipo iye anati, Turuka, nuime pa phiri tino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikuru ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhala m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali cibvomezi; komanso Yehova sanali m'cibvomezico.

12. Citaleka cibvomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo, Utaleka mota panali bata la kamphepo kayaziyazi.

13. Ndipo atamva Eliya, anapfunda nkhope yace ndi copfunda cace, naturuka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Ucitanji kuno, Eliya?

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 19