Ndipo anati, Ine ndinacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli anasiya cipangano canu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.