Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 11:23-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wace Hadadezeri mfumu ya ku Zoba.

24. Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, hakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.

25. Ndipo iye anali mdani wa Israyeli masiku onse a Solomo, kuonjezerapo coipa anacicita Hadadi, naipidwa nao Aisrayeli, nakhala mfumu ya ku Aramu.

26. Ndipo Yerobiamu mwana wa Nebati M-efrati wa ku Zereda mnyamata wa Solomo, dzina la amace ndiye Zeruwa, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lace pa mfumu.

27. Ndipo cifukwa cakukweza iye dzanja lace pa mfumu ndi cimeneci: Solomo anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wace.

28. Ndipo munthu ameneyo Yerobiamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomo anamuona mnyamatayo kuti ngwacangu, anamuika akhale woyang'anira wa nchito yonse ya nyumba ya Yosefe.

29. Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobiamu anaturuka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anabvaliratu cobvala catsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo.

30. Ndipo Ahiyayo anagwira cobvala cace catsopano, nacing'amba khumi ndi pawiri.

31. Nati kwa Yerobiamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomo ndi kukupatsa iwe mafuko khumi.

32. Koma iye adzakhala nalo pfuko limodzi, cifukwa ca Davide mtumiki wanga, ndi ca Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israyeli.

33. Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Azidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amoabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kucita cimene ciyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wace.

34. Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lace, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ace onse, cifukwa ca Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, cifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.

35. Koma ndidzalanda ufumu m'dzanja la mwana wace, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene.

36. Ndipo ndidzamninkha mwana wace pfuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale cikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa.

37. Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzacita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israyeli.

38. Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kucita cilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga nelinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 11