Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 10:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji, ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikanso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi inapereka kwa mfumu Solomo.

11. Ndipo zombe za Hiramu zotengera golidi ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali.

12. Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oyimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.

13. Ndipo mfumu Solomo ananinkha mfumu yaikazi ya ku Seba cifuniro cace conse anacipempha iye, osawerenga cimene Solomo anamninkha mwa ufulu waceo Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lace, iyeyo ndi anyamata ace.

14. Tsono kulemera kwace kwa golidi anafika kwa Solomo caka cimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi liimodzi a golidi,

15. osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabu, ndi wa akazembe onse a madera.

16. Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri zagolidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.

17. Ndi malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, libawo limodzi linapangidwa ndi miyeso itatu ya golidi; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.

18. Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wacifumu waminyanga, naukuta ndi golidi woyengetsa.

19. Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.

20. Ndipo anaimikamikango khumi ndi iwiri mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko liri lonse tina simunapangidwa wotere.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 10