Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 22:24-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. ndipo ngati ife sitinacita ici cifukwa ca kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli ciani inu kwa Yehova Mulungu wa Israyeli?

25. pakuti Yehova anaika Yordano ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope. Yehova.

26. Cifukwa cace tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;

27. koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu; ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikacita nchito ya Yehova pamaso pace ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.

28. Cifukwa cace tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, citsanzo ca guwa la nsembe la Yehova, comanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.

29. Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa cihema cace.

30. Pamene Pinehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akuru a mabanja a Israyeli okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.

31. Ndipo Pinehasi, mwana wa Eleazare wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, Lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira naco Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israyeli m'dzanja la Yehova.

32. Ndipo Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe, ndi akalonga anabwerera kucokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Gileadi, kudza ku dziko La Kanani kwa ana a Israyeli, nawabwezera mau.

33. Ndipo mauwo anakomera ana a Israyeli pamaso pao; ndi ana a Israyeli analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi.

34. Ndipo ana a Rubeni ndi: ana a Gadi analicha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 22