Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Munthu wobadwa ndi mkaziNgwa masiku owerengeka, nakhuta mabvuto,

2. Aturuka ngati duwa, nafota;Athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3. Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,Ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4. Adzaturutsa coyera m'cinthu codetsa ndani? nnena mmodzi yense.

5. Popeza masiku ace alembedwa, ciwerengo ca miyezi yace cikhala ndi Inu,Ndipo mwamlembera malire ace, kuti asapitirirepo iye;

6. Mumleke osamthira maso, kuti apumule,Kuti akondwere nalo tsiku lace monga wolembedwa nchito.

7. Pakuti akaulikha mtengo pali ciyembekezo kuti udzaphukanso,Ndi kuti nthambi yace yanthete siidzasowa.

8. Ngakhale muzu wace wakalamba m'nthaka,Ndi tsinde lace likufa pansi;

9. Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka,Nudzaswa nthambi ngati womera.

10. Koma munthu akufa atacita liondeondeInde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti?

11. Madzi acoka m'nyanja,Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12. Momwemo munthu agona pansi, osaukanso;Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,Kapena kuutsidwa pa tulo tace.

13. Ha! mukadandibisa kumanda,Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,Mpaka kwafika kusandulika kwanga,

15. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;Mukadakhumba nchito ya manja anu.

16. Koma tsopano muwerenga maponda mwanga;Kodi simuyang'anitsa cimo langa?

17. Colakwa canga caikidwa m'thumba lokomedwa cizindikilo;Ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18. Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;Ndi thanthwe lisunthika m'malo mwace;

19. Madzi anyenya miyala;Zosefukira zao zikokolola pfumbi la nthaka;Ndipo muononga ciyembekezo ca munthu.

20. Mumlaka cilakire, napita iye;Musintha nkhope yace, mumuuza acoke.

21. Ana ace aona ulemu osadziwa iye;Napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.

22. Koma thupi lace limuwawira yekha,Ndi mtima wace umliritsa yekha.