Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,Kumanda kwandikonzekeratu.

2. Zoonadi, ali nane ondiseka;Ndi diso langa liri cipenyere m'kundiwindula kwao.

3. Mupatse cigwiriro tsono, mundikhalire cikole Inu nokha kwanu;Ndani adzapangana nane kundilipirira?

4. Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;Cifukwa cace simudzawakuza.

5. Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo,M'maso mwa ana ace mudzada.

6. Anandiyesanso nthanthi za anthu;Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace.

7. M'diso mwanga mucita cizirezire cifukwa ca cisoni,Ndi ziwalo zanga zonse ziribe cithunzi.

8. Anthu oongoka mtima adzadabwa naco,Ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsotsa wonyoza Mulunguyo.

9. Koma wolungama asungitsa njira yace,Ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.

10. Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;Pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.

11. Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,Zace zace zomwe za mtima wanga.

12. Zisanduliza usiku ukhale usana;Kuunika kuyandikana ndi mdima.

13. Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;Ndikayala pogona panga mumdima.

14. Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;Kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;

15. Ciri kuti ciyembekezo canga?Inde, ciyembekezo canga adzaciona ndani?

16. Cidzatsikira ku mipingiridzo ya kumanda,Pamene tipumulira pamodzi kupfumbi.