Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Elihu akuti kwa Mulungu kulibe cifukwa ca kucita tsankhu

1. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2. Kodi muciyesa coyenera,Umo mukuti, Cilungamo canga ciposa ca Mulungu,

3. Pakuti munena, Upindulanji naco?Posacimwa ndinapindula ciani cimene sindikadapindula pocimwa?

4. Ndidzakuyankhani,Ndi anzanu pamodzi ndi inu.

5. Yang'anani kumwamba, nimuone,Tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.

6. Ngati mwacimwa, mumcitira Iye ciani?Zikacuruka zolakwa zanu, mumcitira Iye ciani?

7. Mukakhala wolungama, mumninkhapo ciani?Kapena alandira ciani pa dzanja lanu?

8. Coipa canu cikhoza kuipira munthu wonga inu,Ndi cilungamo canu cikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.

9. Cifukwa ca kucuruka masautso anthu anapfuula,Apfuula cifukwa ca dzanja la amphamvu.

10. Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga,Wakupatsa nyimbo usiku;

11. Wakutilangiza ife koposa nyama za padziko,Wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?

12. Apo apfuula, koma Iye sawayankha;Cifukwa ca kudzikuza kwa anthu oipa.

13. Zedi Mulungu samvera zacabe,Ndi Wamphamvuyonse sazisamalira.

14. Inde mungakhale munena, Sindimpenya,Mlanduwo uli pamaso pace, ndipo mumlindira.

15. Ndipo tsopano popeza analibe kumzonda m'kukwiya kwace,Ndi kusamalitsa colakwa,

16. Cifukwa cace Yobu anatsegula pakamwa pace mwacabe,Nacurukitsa mau opanda nzeru.