Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Yobu abwereza kukana kuti sanacimwa. Mulungu wosadziwika acita cifuniro cace. Kwambiri ocimwa oyenera kulangidwa akhala bwino m'moyo uno

1. Koma Yobu anayankha, nati,

2. Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;Kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwace.

3. Ha! ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,Kuti ndifike ku mpando wace!

4. Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pace,Ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano.

5. Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,Ndikadazindikira cimene akadanena nane.

6. Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?Iai, koma akadandicherera khutu.

7. Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.

8. Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;Kapena m'mbuyo sindimzindikira;

9. Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;Akabisala kulamanja, sindimuona,

10. Koma adziwa njira ndilowayi;Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.

11. Phazi langa lagwiratu moponda Iye,Ndasunga njira yace, wosapambukamo.

12. Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.

13. Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?Ndi ici cimene moyo wace ucifuna acicita.

14. Pakuti adzacita condiikidwiratu;Ndipo zambiri zotere ziri ndi Iye.

15. Cifukwa cace ndiopsedwa pankhope pace;Ndikalingirira, ndicita mantha ndi Iye.

16. Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,Ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.