Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Yobu atsutsa Bilidadi kuti sanamthandiza; yekha nalemekeza ukulu wa Mulungu

1. Koma Yobu anayankha, nati,

2. Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu,Kulipulumutsa dzanja losalimba!

3. Wampangira bwanji wopanda nzeruyu!Ndi kudziwitsa nzeru zeni zeni mocurukal

4. Wafotokozera yani mau?Ndi mzimu wa yani unaturuka mwa iwe?

5. Adafawo anjenjemeraPansi pa madzi ndi zokhalamo,

6. Kumanda kuli padagu pamaso pace,Ndi kucionongeko kusowa cophimbako,

7. Ayala kumpoto popanda kanthu, Nalenjeka dziko pacabe.

8. Amanga madzi m'mitambo yace yocindikira;Ndi mtambo sung'ambika pansi pace,

9. Acingira pa mpando wace wacifumu,Nayalapo mtambo wace.

10. Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.

11. Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.

12. Mwa mphamvu yace agwetsa nyanja bata;Ndipo mwa luntha lace akantha kudzikuza kwace.

13. Mwa mzimu wace anyezimiritsa thambo;Dzanja lace linapyoza njoka yothawayo.

14. Taonani, awa ndi malekezero a njira zace;Ndi cimene tikumva za Iye ndi cinong'onezo cacing'ono;Koma kugunda kwa mphamvu yace akuzindikiritsa ndani?