Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 65:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene Ine sindinakondwera naco.

13. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;

14. taonani, atumiki anga adzayimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wacisoni; ndipo mudzapfuula cifukwa ca kusweka mzimu.

15. Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale citemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzacha atumiki ace dzina lina;

16. comweco iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zobvuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.

17. Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwa tsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.

18. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthawi zonse ndi ici ndicilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ace okondwa.

19. Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akupfuula.

20. Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ace; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wocimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatembereredwa.

21. Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzanka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zace.

22. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzanka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhalamasiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi nchito za manja ao.

23. Iwo sadzagwira nchito mwacabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbeu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa ao adzakhala pamodzi ndi iwo.

24. Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali cilankhulire, Ine ndidzamva.

25. Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi pfumbi lidzakhala cakudya ca njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 65