Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 49:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;

6. inde, ati, Ciri cinthu copepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale cipulumutso canga mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

7. Atero Yehova, Mombolo wa Israyeli, ndi Woyera wace, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyansidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira cifukwa ca Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israyeli, amene anakusankha Iwe.

8. Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la cipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;

9. ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti se mudzakhala busa lao.

10. Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawacitira cifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.

11. Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka.

12. Taonani, awa adzacokera kutari; ndipo taonani, awa ocokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ocokera ku dziko la Sinimu.

13. Yimbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, yimbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, nadzacitira cifundo obvutidwa ace.

14. Koma Ziyoni anati, Yehova wandisiya ine, ndipo Ambuye wandiiwala ine.

15. Kodi mkazi angaiwale mwana wace wa pabere, kuti iye sangacitire cifundo mwana wombala iye? inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.

16. Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga,

17. Ana ako afulumira; opasula ako ndi iwo amene anakusakaza adzacoka pa iwe.

18. Tukula maso ako kuunguza-unguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadzibveka wekha ndi iwo onse, monga ndi cokometsera, ndi kudzimangira nao m'cuuno ngati mkwatibwi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 49