Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 44:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wina adzati, Ine ndiri wa Yehova; ndi wina adzadzicha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lace, Ndine wa Yehova, ndi kudzicha yekha ndi mfunda wa lsrayeli.

6. Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

7. Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ici ndi kundilongosolera ici, cikhazikitsire Ine anthu akale? milunguyo iwadziwitse zomwe zirinkudza, ndi za m'tsogolo.

8. Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa liri lonse.

9. Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.

10. Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?

11. Taonani anzace onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ace ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi.

12. Wacipala acita zace ndi nsompho, nagwira nchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira nchito yace ndi mkono wace wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zace zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.

13. Mmisiri wa mitengo atambalitsa cingwe; nalilemba ndi colembera, nalikonza ndi ncerero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.

14. Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.

15. Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naoca mkate; inde, apanga mlungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 44