Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 30:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Katundu wa zirombo za kumwera.M'dziko lobvuta ndi lopweteka, kumeneko kucokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula cuma cao pamsana pa aburu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamila, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.

7. Pakuti thangata la Aigupto liri lacabe, lopanda pace; cifukwa cace ndamucha wonyada, wokhala cabe.

8. Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe ku nthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.

9. Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva cilamulo ca Yehova;

10. amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;

11. cokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israyeli pamaso pathu.

12. Cifukwa cace atero Woyera wa Israyeli, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo;

13. cifukwa cace kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitari, kugumuka kwace kufika modzidzimutsa dzidzidzi.

14. Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zace phale lopalira moto pacoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.

15. Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israyeli, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala cete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.

16. Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; cifukwa cace inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; cifukwa cace iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.

17. Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.

18. Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

19. Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.

20. Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu cakudya ca nsautso, ndi madzi a cipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;

21. ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 30