Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 44:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. popeza muutsa mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu, pofukizira milungu yina m'dziko la Aigupto, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale citemberero ndi citonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?

9. Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazicita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu?

10. Sanadzicepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'cilamulo canga, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

11. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikucitireni inu coipa, ndidule Yuda lonse.

12. Ndipo ndidzatengaotsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Aigupto akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Aigupto adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkuru, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo.

13. Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Aigupto, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola;

14. kuti otsala a Yuda, amene ananka ku dziko la Aigupto kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere ku dziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.

15. Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu yina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukuru, anthu onse okhala m'dziko la Aigupto, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,

16. Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe.

17. Koma tidzacita ndithu mau onse anaturuka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikacitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akuru athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi cakudya cokwanira, tinakhala bwino, sitinaona coipa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 44