Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 41:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali mwezi wacisanu ndi ciwiri, Ismayeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkuru wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa.

2. Ndipo anauka Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babulo inamuika wolamulira dziko.

3. Ismayeli naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Akasidi amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo.

4. Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa,

5. anadza anthu ocokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndebvu zao, atang'amba zobvala zao, atadzitematema, ana tenga nsembe zaufa ndi zonunkhira m'manja mwao, kunka nazo ku nyumba ya Yehova.

6. Ndipo Ismayeli mwana wa Netaniya anaturuka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wace wa Ahikamu.

7. Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismayeli mwana, wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8. Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismayeli, Musatiphe ife; pakuti tiri ndi cuma cobisika m'mudzi, ca tirigu, ndi ca barele, ndi ca mafuta, ndi ca uci. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 41