Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismayeli, Musatiphe ife; pakuti tiri ndi cuma cobisika m'mudzi, ca tirigu, ndi ca barele, ndi ca mafuta, ndi ca uci. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.