Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 38:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namturutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.

14. Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, natntenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lacitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.

15. Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? ndipo ndikakupangirani, simudzandimveta ine.

16. Ndipo Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.

17. Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ngati mudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;

18. koma ngati simudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Akasidi, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.

19. Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Akasidi, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.

20. Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, comweco kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.

21. Koma ngati mukana kuturuka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:

22. Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzaturutsidwa kunka kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.

23. Ndipo adzaturutsira Akasidi akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babulo; ndipo mudzatenthetsa mudziwu ndi moto.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 38