Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 36:18-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pace anandichulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m'bukumo.

19. Ndipo akuru anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli.

20. Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m'cipinda ca Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m'makutu a mfumu.

21. Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kuturuka nao m'cipinda ca Elisama mlembi, Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akuru onse amene anaima pambali pa mfumu.

22. Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yacisanu mwezi wacisanu ndi cinai; ndipo munali moto m'nkhumbaliro pamaso pace.

23. Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'nkhumbaliromo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'nkhumbaliromo.

24. Ndipo sanaopa, sanang'ambe nsaru zao, kapena mfumu, kapena atumiki ace ali yense amene anamva mau onsewa.

25. Tsononso Elinatani ndi Deliya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera.

26. Ndipo mfumu inauza Yeremeeli mwana wace wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Azirieli, ndi Selemiya mwana wa Abidieli, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.

27. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti,

28. Tenganso mpukutu wina, nulembe m'menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.

29. Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babulo idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nvama?

30. Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wacifumu wa Davide; ndipo mtembo wace udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli cisanu.

31. Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zace ndi atumiki ace cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvera.

32. Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 36