Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 33:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za nyumba za mudzi uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwacinjirizire mitumbira, ndi lupanga:

5. Adza kumenyana ndi Akasidi, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga cifukwa ca zoipa zao zonse.

6. Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuciritsa, ndi kuwaciritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kucuruka kwa mtendere ndi zoona.

7. Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israyeli, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja,

8. Ndipo ndidzawayeretsa kucotsa mphulupulu yao, imene anandicimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandicimwira, nandilakwira Ine.

9. Ndipo ndidzayesa mudzi uno cifukwa ca kukondwa, ndi ciyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawacitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira cifukwa ca zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzaucitira.

10. Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'midzi ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama,

11. mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, cifundo cace ncosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12. Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'midzi yace yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13. M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kucidikha, m'midzi ya ku Mwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 33