Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 33:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, cifundo cace ncosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.

12. Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'midzi yace yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.

13. M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kucidikha, m'midzi ya ku Mwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.

14. Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israyeli ndi za nyumba ya Yuda.

15. Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukitsira Davide mphukira ya cilungamo; ndipo adzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dzikomu.

16. Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzachedwa nalo, Yehova ndiye cilungamo cathu.

17. Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wacifumu wa nyumba ya Israyeli;

18. ndiponso ansembe sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakucita nsembe masiku onse.

19. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,

20. Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku m'nyengo yao;

21. pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wace; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 33