Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mcenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; comweco ndidzacurukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.