Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 31:28-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzyala, ati Yehova.

29. Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.

30. Koma yense adzafa cifukwa ca mphulupulu yace; yense amene adya mphesa zowawa, mano ace adzayayamira.

31. Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya lsrayeli, ndi nyumba ya Yuda;

32. si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.

33. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika cilamulo canga m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzacilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

34. ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wace, ndi yense mbale wace, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira cimo lao.

35. Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ace agabvira; Yehova wa makamu ndi dzina lace:

36. Ngati malembawa acoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israyeli idzaleka kukhala mtundu pamaso panga ku nthawi zonse.

37. Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzacotsa mbeu zonse za Israyeli cifukwa ca zonse anazicita, ati Yehova.

38. Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mudziwu udzamangidwira Yehova kuyambira pa nsanja ya Hananeli kufikira ku cipata ca kungondya.

39. Ndipo cingwe coyesera cidzaturukanso kulunjika ku citunda ca Garebi, ndipo cidzazungulira kunka ku Goa.

40. Ndipo cigwa conse ca mitembo, ndi ca phulusa, ndi minda yonse: kufikira ku mtsinje wa Kidroni, kufikira kungondya kwa cipata ca akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse ku nthawi zamuyaya.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 31