Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! ati Yehova.

2. Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipitikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa nchito zanu, ati Yehova.

3. Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipitikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso ku makola ao; ndipo zidzabalana ndi kucuruka.

4. Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.

5. Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzacita mwanzeru, nadzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dziko lino.

6. Masiku ace Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israyeli adzakhala mokhazikika, dzina lace adzachedwa nalo, ndilo Yehova ndiye cilungamo cathu.

7. Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto;

8. koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israyeli kuwaturutsa m'dziko la kumpoto, ndi ku maiko onse kumene ndinawapitikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.

9. Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; cifukwa ca Yehova, ndi cifukwa ca mau ace opatulika.

10. Pakuti dziko ladzala ndi acigololo; pakuti cifukwa ca temberero dziko lilira, mabusa a kucipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siiri yabwino.

11. Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

12. Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.

13. Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasokeretsa anthu anga Israyeli.

14. Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.

15. Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23