Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.