Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 11:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko mayenda mkaka ndi uci, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.

6. Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwacita.

7. Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.

8. Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.

9. Ndipo Yehova anati kwa ine, Ciwembu caoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu.

10. Abwerera kucitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu yina kuti aitumikire; nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.

11. Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo coipa, cimene sangathe kucipulumuka; ndipo adzandipfuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.

12. Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzapfuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.

13. Pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira camanyazi, alingana ndi kucuruka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.

14. Cifukwa cace usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andipfuulira Ine m'kusaukakwao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 11