Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 22:30-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo buru anati kwa Balamu, Si ndine buru wako amene umayenda wokwera pa ine ciyambire ndiri wako kufikira lero lino? Kodi ndikakucitira cotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.

31. Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola liri kudzanja, ndipo anawerama mutu wace, nagwa nkhope yace pansi.

32. Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji buru wako katatu tsopano? taona, ndaturuka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa camtu pamaso panga;

33. koma buru anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.

34. Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndacimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati cikuipirani, ndibwerera.

35. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okha okha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene, Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.

36. Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamturukira kukakomana naye ku mudzi wa Moabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ace.

37. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumiza kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? sindikhoza kodi kukucitira ulemu?

38. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndiri nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.

39. Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati Huzoti.

40. Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.

41. Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera nave ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.

Werengani mutu wathunthu Numeri 22