Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola liri kudzanja, ndipo anawerama mutu wace, nagwa nkhope yace pansi.