Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.

9. Izi ndi zako pa zinthu zopatulikitsa, zosafika kumoto; zopereka: zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zaucimo, ndi nsembe zao zonse zoparamula, zimene Andibwezera Ine, zikhale zopatulikitsa za iwe ndi za ana ako amuna.

10. Muzizidya izi monga zopatulikitsa; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika.

11. Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israyeli; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.

12. Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa, zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.

13. Zipatso zoyamba zonse ziri m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.

14. Ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zako.

15. Ziri zonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18