Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 8:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Ezara wansembe anabwera naco cilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri.

3. Nawerenga m'menemo pa khwalala liri ku cipata ca kumadzi kuyambira mbanda kuca kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anacherera khutu buku la cilamulo.

4. Ndipo Ezara mlembi anaima pa ciunda ca mitengo adacimangira msonkhanowo; ndi pambali: pace padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseya, ku dzanja lamanja lace; ndi ku dzanja lamanzere Pedaya, ndi Misayeli, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.

5. Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.

6. Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkuru. Nabvomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi.

7. Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodayi, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu cilamuloco; ndi anthu anali ciriri pamalo pao,

8. Nawerenga iwo m'buku m'cilamulo ca Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa cowerengedwaco.

9. Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamacita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a cilamulo.

10. Nanena naonso, Mukani mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lace iye amene sanamkonze ratu kanthu; cifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamacita cisoni; pakuti cimwemwe ca Yehova ndico mphamvu yanu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 8