Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 17:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. kotero kuti ana a Israyeli azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.

6. Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la cihema cokomanako, natenthe mafuta akhale pfungo lokoma lokwera kwa Yehova.

7. Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.

8. Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,

9. osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

10. Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

11. Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.

12. Cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo ali yense wakugoneramwa inu asamadya mwazi.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 17