Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:15-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yaucimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wace m'tseri mwa nsaru yocinga, nacite nao mwazi wace monga umo anacitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pacotetezerapo ndi cakuno ca cotetezerapo;

16. nacitire cotetezera malo opatulika, cifukwa ca kudetsedwa kwa ana a Israyeli, ndi cifukwa ca zolakwa zao, monga mwa zocimwa zao zonse; nacitire cihema cokomanako momwemo, cakukhala nao pakati pa zodetsa zao.

17. Ndipo musakhale munthu m'cihema cokomanako pakulowa iye kucita cotetezera m'malo opatulika, kufikira aturuka, atacita cotetezera yekha, ndi mbumba yace, ndi msonkhano wonse wa Israyeli.

18. Ndipo aturukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulicitira cotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

19. Ndipo awazepo mwazi wina ndi cala cace kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulicotsera zodetsa za ana a Israyeli.

20. Ndipo atatha kucitira cotetezera malo opatulika, ndi cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16