Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 22:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano.

2. Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.

3. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga buru wace, natengako anyamata ace awiri pamodzi naye, ndi Isake mwana wace, nawaza nkhuni za nsembe, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye,

4. Tsiku lacitatu Abrahamu anatukula maso ace naona malowo patari.

5. Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ace, Khalani kuno ndi buru, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.

6. Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isake mwana wace; natenga mota m'dzanja lace ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri.

7. Ndipo Isake ananena ndi Abrahamu atate wace, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?

8. Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.

9. Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isake mwana wace, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.

10. Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lace, natenga mpeni kuti amuphe mwana wace.

11. Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano.

12. Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamcitire iye kanthu; cifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.

13. Ndipo Abrahamu anatukula maso ace nayang'ana taonani, pambuyo pace nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zace m'ciyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wace.

14. Ndipo Abrahamu anacha dzina lace la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova cidzaoneka.

15. Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kaciwiri,

Werengani mutu wathunthu Genesis 22