Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.