Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 10:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya. Mulungu, nalowa m'cipinda ca Yehohanana mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadya mkate, sanamwa madzi; pakuti anacita maliro cifukwa ca kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.

7. Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;

8. ndi kuti ali yense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akuru, cuma cace conse cidzaonongeka konse, ndipo iye adzacotsedwa ku msonkhano wa iwo otengedwa ndende.

9. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wacisanu ndi cinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera cifukwa ca mlandu uwu, ndi cifukwa ca mvulayi.

10. Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi acilendo, kuonjezera kuparamula kwa Israyeli.

11. Cifukwa cace tsono, ululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimucite comkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi acilendo.

12. Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akuru, Monga mwa mau anu tiyenera kucita.

13. Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tiribenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi nchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tacurukitsa kulakwa kwathu pa cinthu ici.

Werengani mutu wathunthu Ezara 10