Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 10:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israyeli msonkhano waukuru ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira, kwakukuru.

2. Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyeli, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi acilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano cimtsalira Israyeli ciyembekezo kunena za cinthu ici.

3. Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kucotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo cicitike monga mwa cilamulo.

4. Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tiri nanu; limbikani, citani.

5. Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisrayeli onse, kuti adzacita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.

6. Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya. Mulungu, nalowa m'cipinda ca Yehohanana mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadya mkate, sanamwa madzi; pakuti anacita maliro cifukwa ca kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.

7. Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;

8. ndi kuti ali yense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akuru, cuma cace conse cidzaonongeka konse, ndipo iye adzacotsedwa ku msonkhano wa iwo otengedwa ndende.

Werengani mutu wathunthu Ezara 10