Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyeli, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi acilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano cimtsalira Israyeli ciyembekezo kunena za cinthu ici.