Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 2:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lace, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m'cinyumba ca ku Susani, awasunge Hege, anamtenga Estere yemwe, alowe m'nyumba ya mfumu, amsunge Hege wosunga akazi.

9. Ndipo namwaliyo anamkomera, namcitira cifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zace zomyeretsa, ndi magawo ace, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ocokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ace akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.

10. Estere sadaulula mtundu wace ndi cibale cace; pakuti Moredekai adamuuzitsa kuti asadziulule.

11. Ndi Moredekai akayendayenda tsiku ndi tsiku ku bwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi cimene cidzamcitikira.

12. Kunafika tsono kulowa kwace kwa namwali ali yense, kuti alowe kwa mfumu Ahaswero, atamcitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti adafokwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi.

13. Ndipo namwali ali yense analowa kwa mfumu matero, ziri zonse anafuna anampatsa zocokera m'nyumba ya akazi, alowe nazo ku nyumba ya mfumu.

14. Madzulo ace analowamo, nabwera m'mawa mwace kumka ku nyumba yaciwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi ang'ono a mfumu; iyeyu sanakwanso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumchula dzina lace, ndiko.

15. Pofika tsono kulowa kwace kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Moredekai, amene adadzitengera akhale mwana wace, kuti alowe kwa mfumu, sanafuna kanthu koma zonena Hege mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya.

16. Momwemo anatengedwa Estere kumka kwa mfumu Ahaswero, ku nyumba yace yacifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebete, caka cacisanu ndi ciwiri ca ufumu wace.

Werengani mutu wathunthu Estere 2