Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wace wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wace ndi mai wace, Moredekai anamtenga akhale mwana wace.