Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 4:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa comwe ukalankhule.

13. Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma.

14. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, aturuka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondweram'mtima mwace.

15. Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwace, ndipo ndidzakuphunzitsani inu cimene mukacite.

16. Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.

17. Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukacite nayo zizindikilozo.

18. Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wace, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kumka kwa abale anga amene ali m'Aigupto, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.

19. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'Midyani, Muka, bwerera kumka ku Aigupto; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.

20. Pamenepo Mose anatenga mkazi wace ndi ana ace amuna, nawakweza pa buru, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 4