Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire ucite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wace kuti asadzalole anthu kupita.