Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 7:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.

10. Ndipo awabwezera onse akudana ndi iye, pamaso pao, kuwaononga; sacedwa naye wakudana ndi iye, ambwezera pamaso pace.

11. Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo, amene ndikuuzani lero kuwacita.

12. Ndipo kudzakhala, cifukwa ca kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwacita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani cipangano ndi cifundo cimene analumbirira makolo anu;

13. ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukucurukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi ana a nkhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.

14. Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.

15. Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.

16. Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawacitire cifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakucitirani msampha.

17. Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andicurukira; ndikhoza bwanji kuwapitikitsa?

18. musamawaopa; mukumbukile bwino cimene Yehova Mulungu wanu anacitira Farao, ndi Aigupto wonse;

19. mayesero akuru maso anu anawapenya, ndi zizindikilo ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakuturutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.

20. Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mabvu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.

21. Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkuru ndi woopsa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 7