Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.