Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 16:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paskha, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lace.

3. Musamadyera nayo mkaye wa cotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda cotupitsa, ndiwo mkate wa cizunziko popeza munaturuka m'dziko la Aigupto mofulumira; kuti inu kumbukile tsiku loturuka inu m'dziko la Aigupto masiku onse a moyo wanu.

4. Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke cotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.

5. Simuyenera kuphera nsembe ya Paskha m'midzi yanu iri yonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani;

6. koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lace, pamenepo muphere nsembe ya Paskha, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kuturuka inu m'Aigupto.

7. Ndipo muiphike ndi kuidya m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; koma m'mawa mwace mubwerere kumka ku mahema anu.

8. Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda cotupitsa; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira nchito pamenepo.

9. Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kuceka tirigu waciriri.

10. Ndipo mucitire Yehova Mulungu wanu madyerero a masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani.

11. Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi anchito anu amuna, ndi anchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.

12. Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'Aigupto; musamalire kucita malemba awa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 16